17 Ahaziya anamwaliradi mogwirizana ndi mawu a Yehova amene Eliya ananena. Ndipo chifukwa choti analibe mwana wamwamuna, Yehoramu+ anakhala mfumu mʼmalo mwake. Iye anayamba kulamulira mʼchaka chachiwiri cha Yehoramu+ mwana wa Yehosafati mfumu ya Yuda.