16 Ndiyeno ana a aneneriwo anauza Elisa kuti: “Ife atumiki anu tili ndi amuna 50 amphamvu. Bwanji tiwatume kukafunafuna mbuye wanu? Mwina mzimu wa Yehova wamunyamula ndipo wamʼponya paphiri linalake kapena mʼchigwa.”+ Koma Elisa anayankha kuti: “Ayi musawatume.”