13 Elisa anafunsa mfumu ya Isiraeli kuti: “Mukufuna chiyani kwa ine?+ Pitani kwa aneneri a bambo anu ndi kwa aneneri a mayi anu.”+ Koma mfumu ya Isiraeliyo inati: “Ayi musatero, chifukwa Yehova wasonkhanitsa mafumu atatufe kuti atipereke mʼmanja mwa Amowabu.”