27 Choncho mfumu ya Mowabu inatenga mwana wake wamwamuna woyamba kubadwa amene akanalowa ufumu mʼmalo mwake nʼkumupereka nsembe yopsereza+ pakhoma. Atatero anthu anakwiyira kwambiri Aisiraeli ndipo iwo anasiya kumenyana ndi mfumu ya Mowabu nʼkubwerera kwawo.