27 Mayiyo atafika kwa munthu wa Mulungu woona paphiripo, nthawi yomweyo anamʼgwira mapazi.+ Gehazi ataona zimenezo, anabwera pafupi kuti amukankhe mayiyo. Koma munthu wa Mulungu woonayo anamuuza kuti: “Musiye, mtima wake ukumʼpweteka kwambiri. Koma Yehova wandibisira, sanandiuze.”