5 Panali munthu wina dzina lake Namani, yemwe anali mkulu wa asilikali a mfumu ya Siriya. Iye anali munthu wotchuka ndipo mbuye wake ankamulemekeza kwambiri chifukwa Yehova anapulumutsa Asiriya kudzera mwa iyeyo. Namani anali msilikali wamphamvu ngakhale kuti anali wakhate.