17 Kenako Namani anati: “Ngati mukukana, chonde mundipatse ine mtumiki wanu dothi lakuno loti nyulu ziwiri zikhoza kunyamula. Ndikutero chifukwa ine mtumiki wanu sindidzaperekanso nsembe yopsereza kapena nsembe iliyonse kwa milungu ina, koma kwa Yehova basi.