18 Koma Yehova andikhululukire ine mtumiki wanu pa nkhani iyi yokha: Mbuyanga akalowa mʼnyumba ya Rimoni kuti akamugwadire, amatsamira mkono wanga choncho ndimafunika kugwada mʼnyumba ya Rimoni. Ndikagwada mʼnyumba ya Rimoni, chonde Yehova andikhululukire ine mtumiki wanu pa nkhani imeneyi.”