20 Gehazi,+ mtumiki wa Elisa munthu wa Mulungu woona,+ anaganiza mumtima mwake kuti: ‘Zoona mbuyanga wangomusiya Namani wa ku Siriya+ uja osalandira zinthu zomwe anabweretsa? Ndikulumbira mʼdzina la Yehova Mulungu wamoyo, ndimʼthamangira kuti ndikatengeko zinthu zina.’