29 Choncho Mfumu Yehoramu inabwerera ku Yezereeli+ kuti ikachire mabala amene Asiriya anaivulaza ku Rama, pamene inkamenyana ndi Hazaeli mfumu ya Siriya.+ Ahaziya mwana wa Yehoramu mfumu ya Yuda anapita ku Yezereeli kukaona Yehoramu mwana wa Ahabu chifukwa anali atavulazidwa.