15 Kenako Mfumu Yehoramu anabwerera ku Yezereeli+ kuti akachire mabala amene Asiriya anamuvulaza pamene ankamenyana ndi Hazaeli mfumu ya Siriya.+
Ndiyeno Yehu anati: “Ngati mukugwirizana nazo, musalole aliyense kutuluka mumzinda uno nʼkukanena zimenezi ku Yezereeli.”