-
2 Mafumu 12:18Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 Zitatero Yehoasi mfumu ya Yuda anatenga zopereka zonse zopatulika zimene makolo ake Yehosafati, Yehoramu ndi Ahaziya, mafumu a Yuda anaziyeretsa. Anatenganso zopereka za iyeyo zopatulika, ndi golide yense yemwe anali mosungira chuma cha mʼnyumba ya Yehova ndi cha mʼnyumba ya mfumu nʼkuzitumiza kwa Hazaeli mfumu ya Siriya.+ Choncho Hazaeli anabwerera osaukira Yerusalemu.
-