25 Yerobowamu anabwezeretsa malire a Isiraeli kuyambira ku Lebo-hamati+ mpaka kunyanja ya Araba.+ Anachita zimenezi mogwirizana ndi mawu a Yehova Mulungu wa Isiraeli omwe anawalankhula kudzera mwa mtumiki wake Yona+ mwana wa Amitai, mneneri wa ku Gati-heferi.+