-
2 Mafumu 16:15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Ndiyeno Mfumu Ahazi analamula wansembe Uliya+ kuti: “Paguwa lansembe lalikululi uziwotchapo nsembe yopsereza yamʼmawa,+ nsembe yambewu yamadzulo,+ nsembe yopsereza ya mfumu ndi nsembe yake yambewu. Uziwotchaponso nsembe zopsereza za anthu onse amʼdzikoli, nsembe zawo zambewu ndiponso nsembe zawo zachakumwa. Komanso uziwaza paguwali magazi onse a nsembe yopsereza ndi magazi onse a nsembe zina. Koma guwa lansembe lakopalo, ndiona chochita nalo.”
-