49 Aroni ndi ana ake+ ankapereka nsembe zautsi paguwa lansembe zopsereza+ ndi paguwa lansembe zofukiza.+ Ankagwira ntchito zonse zokhudza zinthu zopatulika kwambiri, kuti aphimbe machimo a Aisiraeli,+ mogwirizana ndi zonse zimene Mose mtumiki wa Mulungu woona analamula.