78 Kuchokera ku fuko la Rubeni, anawapatsa mzinda wa Bezeri mʼchipululu ndi malo ake odyetserako ziweto. Mzindawo unali mʼchigawo cha Yorodano pafupi ndi Yeriko chakumʼmawa kwa Yorodano. Anawapatsanso mzinda wa Yahazi+ ndi malo ake odyetserako ziweto,