3 Choncho akulu onse a Isiraeli anabwera kwa mfumu ku Heburoni ndipo Davide anachita nawo pangano ku Heburoniko pamaso pa Yehova. Kenako iwo anadzoza Davide kukhala mfumu ya Isiraeli,+ mogwirizana ndi mawu a Yehova amene analankhula kudzera mwa Samueli.+