19 Iye anati: “Ndikaiona nkhaniyi mmene Mulungu akuionera, sindingachite zimenezi. Kodi ndimwe magazi a amuna amene anaika moyo wawo pa ngoziwa?+ Chifukwa anaika moyo wawo pa ngozi kuti akatunge madziwa.” Choncho iye anakana kumwa madziwo. Izi nʼzimene asilikali ake atatu amphamvuwo anachita.