-
1 Mbiri 12:40Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
40 Ndiponso anthu onse apafupi ndi kumeneko, mpaka kumadera a Isakara, Zebuloni ndi Nafitali, ankabweretsa chakudya pa abulu, ngamila, nyulu* ndi ngʼombe. Anabweretsa zakudya zophikidwa ndi ufa. Anabweretsanso makeke a nkhuyu, makeke a mphesa, vinyo, mafuta, ngʼombe ndi nkhosa. Anabweretsa zambirimbiri chifukwa anthu mu Isiraeli anasangalala kwambiri.
-