6 Patapita nthawi, Aamoni anaona kuti akhala ngati chinthu chonunkha kwa Davide. Choncho Hanuni ndi Aamoni anatumiza anthu nʼkuwapatsira matalente asiliva 1,000 kuti akabwereke magaleta komanso kulemba ganyu asilikali okwera pamahatchi a ku Mesopotamiya, a ku Aramu-maaka ndi a ku Zoba.+