20 Kumayambiriro kwa chaka, pa nthawi imene mafumu ankapita kukamenya nkhondo, Yowabu+ anatsogolera gulu lankhondo nʼkukawononga dziko la Aamoni ndiponso kuzungulira mzinda wa Raba.+ Koma Davide anatsala ku Yerusalemu.+ Yowabu anaukira mzinda wa Raba nʼkuuwononga.+