16 Davide atakweza maso, anaona mngelo wa Yehova ataima mʼmalere atagwira lupanga+ nʼkuloza Yerusalemu ndi lupangalo. Davide ndi akulu amene anali naye anali atavala ziguduli+ ndipo nthawi yomweyo, anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope zawo kufika pansi.+