9 Tamvera, udzabereka mwana.+ Mwana ameneyo adzakhala munthu wokonda mtendere ndipo ndidzachititsa kuti azikhala mwamtendere komanso asamavutitsidwe ndi adani ake omuzungulira.+ Nʼchifukwa chake dzina lake adzakhala Solomo+ ndipo mʼmasiku ake ndidzapatsa Aisiraeli bata ndi mtendere.+