28 Ntchito yawo inali yothandiza ana a Aroni+ pa utumiki wapanyumba ya Yehova, kuyangʼanira mabwalo a nyumbayo,+ zipinda zodyeramo, ntchito yoyeretsa chinthu chilichonse chopatulika ndiponso ntchito iliyonse yofunika potumikira panyumba ya Mulungu woona.