31 Iwonso anachita maere+ ngati mmene abale awo, ana a Aroni, anachitira pamaso pa Mfumu Davide, Zadoki, Ahimeleki ndiponso atsogoleri a nyumba za makolo za ansembe ndi za Alevi. Nyumba ya makolo ya wamkulu inali chimodzimodzi ndi nyumba ya makolo ya wamngʼono.