28 Panalinso zinthu zonse zimene Samueli wamasomphenya,+ Sauli mwana wa Kisi, Abineri+ mwana wa Nera ndi Yowabu+ mwana wa Zeruya+ anaziyeretsa kuti zikhale zopatulika. Chilichonse chimene munthu anachiyeretsa chinkayangʼaniridwa ndi Selomiti ndi abale ake.