-
1 Mbiri 28:1Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
28 Kenako Davide anasonkhanitsa akalonga onse a Isiraeli ku Yerusalemu. Akalongawo anali a mafuko ndi a magulu+ otumikira mfumu, atsogoleri a magulu a anthu 1,000, atsogoleri a magulu a anthu 100+ ndiponso atsogoleri oyangʼanira katundu yense ndi ziweto zonse za mfumu+ ndi za ana ake.+ Panalinso nduna zapanyumba ya mfumu ndiponso mwamuna aliyense wamphamvu ndi wodalirika.+
-