20 Kenako Davide anauza Solomo mwana wake kuti: “Limba mtima ndipo ugwire ntchitoyi mwamphamvu. Usaope kapena kuchita mantha chifukwa Yehova Mulungu, Mulungu wanga, ali nawe.+ Sadzakutaya kapena kukusiya+ mpaka ntchito yonse yokhudza utumiki wa nyumba ya Yehova itatha.