21 Tsopano ndikukupatsa magulu a ansembe+ ndi a Alevi+ ogwira ntchito zonse zapanyumba ya Mulungu woona. Uli ndi amisiri odzipereka komanso aluso amene angagwire ntchito iliyonse+ ndiponso akalonga+ ndi anthu onse amene angatsatire malangizo ako onse.”