21 Anthuwo anayamba kupereka nsembe kwa Yehova ndipo anapereka nsembe zopsereza+ kwa Yehova mpaka tsiku lotsatira. Anapereka ngʼombe zamphongo zazingʼono 1,000, nkhosa zamphongo 1,000, ana a nkhosa amphongo 1,000 ndi nsembe zake zachakumwa.+ Iwo anapereka nsembe zambirimbiri za Aisiraeli onse.+