5 Choncho Solomo anamaliza ntchito yonse yokhudza nyumba ya Yehova+ imene anayenera kugwira. Kenako Solomo anabweretsa zinthu zimene bambo ake Davide anaziyeretsa.+ Anatenga siliva, golide ndiponso zinthu zonse nʼkuziika mosungira chuma chapanyumba ya Mulungu woona.+