-
2 Mbiri 7:6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Ansembe anali ataimirira pamalo awo a ntchito. Nawonso Alevi anaimirira pamalo awo ndipo ananyamula zipangizo zoimbira Yehova nyimbo.+ (Mfumu Davide anapanga zipangizo zimenezi kuti azizigwiritsa ntchito poyamikira Yehova komanso pomutamanda kudzera mwa iwowo,* “chifukwa chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.”) Ansembe ankaimba malipenga+ mokweza patsogolo pawo, Aisiraeli onse ataimirira.
-