7 Solomo anapatula pakati pa bwalo la nyumba ya Yehova kuti aperekerepo nsembe zopsereza+ ndiponso mafuta a nsembe zamgwirizano. Anatero chifukwa paguwa lansembe lakopa+ limene iye anamanga sipakanakwana kuperekerapo nsembe zopsereza,+ nsembe zambewu ndiponso mafuta.+