11 Solomo anatulutsa mwana wamkazi+ wa Farao mu Mzinda wa Davide nʼkukamuika mʼnyumba imene anamʼmangira+ chifukwa iye anati: “Ngakhale kuti ndi mkazi wanga, sakuyenera kumakhala mʼnyumba ya Davide mfumu ya Isiraeli, poti malo alionse amene Likasa la Yehova likukhala ndi oyera.”+