8 Atamandike Yehova Mulungu wanu, amene wasangalala nanu nʼkukuikani pampando wake wachifumu mʼmalo mwa Yehova Mulungu wanu. Chifukwa Mulungu wanu amakonda Isiraeli+ ndipo amafuna kuti akhalepo mpaka kalekale, wakuikani kuti mukhale mfumu kuti muziweruza anthu ndi kuchita chilungamo.”