11 Mfumuyo inagwiritsa ntchito matabwa a mʼbawawo popanga masitepe a nyumba ya Yehova+ komanso a nyumba ya mfumu.+ Inagwiritsanso ntchito matabwawo kupanga azeze ndi zoimbira za zingwe za oimba.+ Matabwa a mʼbawa otere, sanaonekeponso mʼdziko la Yuda.