9 Kodi simunathamangitse ansembe a Yehova,+ omwe ndi mbadwa za Aroni, komanso Alevi? Ndipo kodi simunadziikire ansembe ngati mmene amachitira anthu a mayiko ena?+ Aliyense amene wabwera ndi ngʼombe yaingʼono yamphongo komanso nkhosa zamphongo 7, amakhala wansembe wa zinthu zomwe si milungu.