7 Iye anauza Ayuda kuti: “Tiyeni timange mizindayi ndi mipanda yake ndiponso nsanja.+ Tiikenso mageti ndi mipiringidzo. Dzikoli lidakali mʼmanja mwathu chifukwa tafunafuna Yehova Mulungu wathu. Tamufunafuna ndipo watipatsa mpumulo mʼdziko lonse.” Choncho ntchito yawo yomanga inayenda bwino.+