33 Koma munthu wina anaponya muvi wake chiponyeponye ndipo unakabaya mfumu ya Isiraeli pamalo olumikizira a chovala chake chokhala ndi mamba achitsulo. Choncho mfumuyo inauza woyendetsa galeta lake kuti: “Bwera udzanditulutse mʼbwalo lankhondoli chifukwa ndavulala kwambiri.”+