20 Mʼmawa wa tsiku lotsatira, anthuwo ananyamuka nʼkupita kuchipululu cha Tekowa.+ Ali mʼnjira, Yehosafati anaimirira nʼkunena kuti: “Tamverani inu Ayuda ndi anthu a ku Yerusalemu! Khulupirirani Yehova Mulungu wanu kuti mukhale olimba. Khulupirirani aneneri ake+ kuti zinthu zikuyendereni bwino.”