25 Choncho Yehosafati ndi anthu ake anapita kukatenga zinthu za adani awowo ndipo anapeza zinthu zambiri, zovala ndi zinthu zina zamtengo wapatali. Iwo anayamba kutenga zinthuzo mpaka zina zinawakanika kunyamula.+ Zinthuzo zinalipo zambiri moti anatuta kwa masiku atatu.