13 Koma wayenda mʼnjira ya mafumu a Isiraeli+ nʼkuchititsa kuti Yuda ndi anthu a ku Yerusalemu achite uhule wauzimu+ ngati uhule wa anthu a mʼbanja la Ahabu.+ Waphanso ngakhale azichimwene ako,+ anthu a mʼnyumba ya bambo ako, amene anali abwino kuposa iweyo.