12 Mfumuyo ndi Yehoyada ankapereka ndalamazo kwa anthu amene ankayangʼanira ntchito yokonza nyumba ya Yehova. Anthuwo ankalemba ntchito osema miyala ndi amisiri okonza nyumba ya Yehova+ komanso amisiri a kopa ndi a zitsulo oti akonze nyumba ya Yehova.