20 Mothandizidwa ndi mzimu wa Mulungu, Zekariya mwana wa wansembe Yehoyada+ anaimirira pamalo okwera nʼkuyamba kuuza anthuwo kuti: “Mulungu woona wanena kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani mukuphwanya malamulo a Yehova? Zinthutu sizikukuyenderani bwino. Poti mwamusiya Yehova, iyenso akusiyani.’”+