23 Kumayambiriro kwa chaka chotsatira, asilikali a ku Siriya anabwera kudzamenyana ndi Yehoasi, ndipo analowa mu Yuda ndi Yerusalemu.+ Asilikaliwo anapha akalonga onse+ ndipo zinthu zonse zimene anatenga kumeneko anazitumiza kwa mfumu ya ku Damasiko.