4 Koma ana awo sanawaphe. Anachita mogwirizana ndi zimene zinalembedwa mʼChilamulo, mʼbuku la Mose, pamene Yehova analamula kuti: “Abambo asamaphedwe chifukwa cha zimene ana awo achita ndipo ana asamaphedwe chifukwa cha zimene abambo awo achita. Munthu aliyense aziphedwa chifukwa cha tchimo lake.”+