-
2 Mbiri 25:16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
16 Mneneriyo atanena zimenezi, mfumuyo inamufunsa kuti: “Kodi tinakuika kuti ukhale mlangizi wa mfumu?+ Usiyiretu kunena zimenezi.+ Ukufuna kuti akuphe?” Choncho mneneriyo anasiya, koma anati: “Ndikudziwa kuti Mulungu wakonza zoti akuwonongeni chifukwa cha zimene mwachitazi ndiponso chifukwa simunamvere malangizo anga.”+
-