-
2 Mbiri 25:18Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 Yehoasi mfumu ya Isiraeli atamva anayankha Amaziya mfumu ya Yuda kuti: “Chitsamba chaminga cha ku Lebanoni chinatumiza uthenga kwa mtengo wa mkungudza wa ku Lebanoni wakuti, ‘Ndipatse mwana wako wamkazi kuti mwana wanga wamwamuna amukwatire.’ Koma nyama yakutchire ya ku Lebanoni inadutsa pamenepo nʼkupondaponda chitsamba chamingacho.
-