10 Iye anamanganso nsanja+ mʼchipululu ndipo anakumba zitsime zambiri (popeza anali ndi ziweto zambiri). Anapanganso zomwezo ku Sefela ndi kudera lafulati. Anali ndi alimi komanso anthu osamalira minda ya mpesa kumapiri ndi ku Karimeli poti iye ankakonda ulimi.