5 Choncho Yehova Mulungu wake anamʼpereka mʼmanja mwa mfumu ya Siriya+ moti Asiriya anamʼgonjetsa ndipo anagwira anthu ambiri nʼkupita nawo ku Damasiko.+ Komanso Mulungu anachititsa kuti Ahazi agonjetsedwe ndi mfumu ya Isiraeli yomwe inapha asilikali ambirimbiri a Ahaziyo.